Bingu wa Muntharika

From Wikipedia

Bingu wa Muntharika, amene anabadwa pa 24 Febuluale 1934, ndi kachenjede wa zachuma (economist), mtsogoleri wa ndale ndiponso Pulezidenti wa dziko la Malawi. A Muntharika anakhala Pulezidenti pa 24 Meyi mchaka ka 2004 pamene anapambana chisankho cha u Pulezidenti chomwe zotsatira zake anthu ena sanazibvomereze.

A Muntharika anapatsidwa dzina loti Brightson Webter Ryson Thom pamene anabadwa ku Thyolo, ma kilomita 30 kuchokera mu mzinda wa Blantyre, iwo anatenganso dzina la ku banja kwawo la Muntharika ndi dzina loyamba la Bingu mu zaka za mma 1960 pamene mayiko a ku Africa anali pa kalikiliki kufuna ufulu wodzilamulira wokha.

Iwowa anayika liu loti ‘wa’ pakati pa mayina awo pofuna kudzibisa kwa anthu a za chitetezo a boma la a Hastings Banda amene ankasaka aliyense owatsutsa pa dziko lonse lapansi. A Muntharika anali mwana wa mphunzitsi wa mkulu wa pa sukulu ya pulayimale. Iwo anakaphunzira ku sukulu ya ukachenjede ya Delhi mu dziko la India kumene anapanga maphunziro a pamwamba a Masters pa nkhani zokhudza chuma. Iwowanso anapanga maphunziro a PhD ku sukulu ya Pacific Western mdziko la United States of America.

Atagwira ntchito m’mboma la Malawi komanso Zambia, a Muntharika anayamba ntchito ku bungwe la dziko lonse la pansi la United Nations mu 1978 kumene anagwira ntchito mpaka kukhala woyang’anira za malonda ndi za chitukuko wa Africa yonse. (Director of Trade and Development for Africa). Iwowa anasankhidwa kukhala wamkulu wa COMESA, gulu la mayiko 20 a mu Africa. A Muntharika anaganiza zokayamba ku United Nations chifukwa ankhatsutsana ndi kudzitchula kwa a Hastings Kamuzu Banda kuti ndi Pulezidenti wamuyaya wa dziko la Malawi. Pamene a Banda anakakamizidwa kuti abvomere ulamuliro wa demokilase, a Mutharika anali m’modzi mwa anthu amene anayambitsa chipani cha United Democratic Front (UDF) chimene chinapambana chisankho choyamba cha zipani za mbiri mu 1994.

Pa nthawi yi, a Muntharika anali wotsatila wa mtsogoleri wa UDF, a Bakili Muluzi koma iwo anayamba kutsutsana ndi zomwe a Muluzi ankachita ku mbali ya za chuma ndipo anachoka mu chipanichi. A Muntharika anayambitsa chipani cha United Party (UP) mu 1997, chomwe chinapanga nawo chisankho chomwe chinachitika m’dzikoli mu 1999, pamene sanapambane.

A Muntharika anathetsa chipani cha UP ndipo analowanso mu UDF atauzidwa kuti akhala wachiwiri kwa Gavanala wa Reserve Bank of Malawi. Iwowa anasankhidwa kukhala nduna yoyang’anira dongosolo la za chuma ndi chitukuko mu 2002 ndiku tchuludwanso ndi a Muluzi kuti akhala wowatsatira pa u Pulezidenti. A Muntharika anapambana ndi 36% ya mavoti a chisankho chomwe chinachitika pa 20 Meyi 2004, ndipo anatsogola kuposa a John Tembo ndi a Gwanda Chakuamba, ndipo anayamba tchitoyi masiku otsatira.

Atakhala Pulizidenti, a Munthaika anakangana ndi a Muluzi, mtsogoleri wa UDF, chifukwa chakuti a Muntharika amatsutsana chi mchitidwe wa chinyengo ndi ziphuphu. Mkangano umenewu unapitilira pa nthawi yonse yomwe a Muntharika anakhala Pulezidenti wa dzikoli, ndipo unafika poyamba kusokokoneza ulamuloro wa dziko. Pa 5 Febuluale 2005, a Muntharika analengeza kuti asiya UDF chifukwa chakuti chipanichi sichimaathandiza ndiponso kubvomerezana nawo pa nkhani yothetsa mchitidwe wa ziphuphu. Zisanachitike izi, kunamvekapo mbiri yakuti a Muntharika achotsedwa mu chipani cha UDF, komanso panali mphekesera yakuti a UDF amafuna kuwapha. Anthu onse amene anakhudzidwa ndi nkhani yofuna kupha a Muntharika anakhululukidwa ndi a Muntharikawo koma iwo anapitiliza kunena za nkhaniyi. A Muntharika anayambitsa chipani chawo cha Demogratic Progressive Movement (DPP).

A Gwanda Chakuamba, amene anali atasankhidwa kukhala nduna ya za ulimi, anachitsedwa ntchitoyi ndi kumangidwa mu Sepitembala 2005 chifukwa chonena kuti a Muntharika adzachoka u Pulezidenti pasanafike pa Khilisimasi. Mu 2006, wachiwiri kwa Pulezidenti a Cassim Chilumpha anamangidwa chifukwa chowaganizira kuti ankafuna kupha a Pulezidenti.

Mu chaka cha 2005, ma nyuzipepala analengeza kuti a Muntharika sakugona ku nyumba ya boma chifukwa cha mizimu yoyipa. Muthu wina wothandizira a Pulezidenti analembedwa kuti aboma anapempha a mipingo kuti achotse mizimuyi. Nkhaniti inakanidwa, ndi a ku nyumba ya boma ndipo atolankhani amene analengeza za nkhaniyi, kuphatikizapo mtolankhani wa BBC anamangidwa. A Muntharika ananena kuti sanayambe akumana ndi mizimu ndipo samayiwopa.

A Muntharika akhala akulimbikitsa kuwakumbukira a Hastings Banda ngati munthu amene anachita za bwino ku dziko la Malawi ndipo mu Meyi 2006 anatsegulira manda a mtsogoleri wa kaleyu amene kumanga kwake kunali kwa ndalama zoposa US$620,000.

M’mwezi wa Okotobala 2006 a Muntharika analengeza kuti adzayimanso pa chisankho cha Pulezidenti mu chaka cha 2009 poyimira chipani cha DPP. A Muntharikawa ali ndi mchimwene wawo, a Peter Muntharika amene ali wophunzitsa za malamulo ku Washington University m’dziko la United States of America. Mkazi wawo ndi a Ethel Muntharika amene kwawo kweni kweni ndi ku Zimbabwe, ndipo ali ndi mwana amene dzina lake ndi Duwa Muntharika.